Anthu a m'boma la Mchinji apeza mwayi wodziwa zambiri zokhudza ngongole za Malawi Enterprise Development Fund (MEDF) Limited pa msonkhano wodziwitsa anthu womwe wachitikira pa Bua Primary School Lachisanu pa 7th August 2026. Polankhula pamsonkhanowu, Mkulu wa bungwe la MEDF, Kayisi Sadala, wati cholinga cha bungweli si kungopereka ngongole zokha, koma kuthandiza anthu kukhala odziyimira pawokha pa zachuma kudzera m'mabizinesi opindulitsa. "Timapereka ngongole limodzi ndi upangiri wa kasamalidwe ka mabizinesi kuti obwereka athe kugwiritsa ntchito bwino ndalama zomwe alandira.
Tikulimbikitsanso aliyense kubweza ngongole pa nthawi yake chifukwa ndalama zomwe zabwezedwa zimathandiza anthu ena kupezanso mwayi wa ngongole," adatero Sadala. Iwo anafotokozanso kuti MEDF imapereka ngongole za munthu payekha, za magulu komanso za Constituency Development Fund (CDF), ndipo munthu payekha atha kupeza ngongole malire K250 miliyoni kwacha kutengera mtundu wa bizinesi ndi kukwaniritsa zofunikira za bungweli.
Poyankhapo, wapampando wa Khonsolo ya Mchinji, Kennedy Peter Chipanga, wapempha anthu kuti aziona ngongole ngati udindo osati mphatso. "Ngongole ziyenera kubwezedwa pa nthawi yake kuti ndalama zomwe zikubwerazi zipitilize kuthandiza anthu ena. Tikufuna anthu agwiritse ntchito bwino mwayiwu kuti mabizinesi awo akule komanso moyo wawo usinthe," adatero Chipanga.
Nayo Inkosi Zulu yapempha MEDF kuti ipitirize kupereka maphunziro a zamabizinesi limodzi ndi ngongole. "Maphunziro ndi ofunika kwambiri chifukwa amathandiza obwereka kuyendetsa bwino mabizinesi awo, kuonjezera phindu komanso kukwanitsa kubweza ngongole pa nthawi yake," yatero Inkosi Zulu. Anthu omwe anapezeka pamsonkhanowu adagwiritsanso ntchito mwayiwu kufunsa mafunso okhudza njira zofunsira ngongole ndi zofunikira kuti ayenere kulandira thandizo la MEDF.