Bungwe la Malawi Enterprise Development Fund (MEDF) linachitsa misonkhano boma la Mzimba yodziwitsa anthu za mitundu ya ngongole komaso ndondomeko zatsopano zotengera ngongole ku bungweli mdera la Khosolo ndi Mpherembe.
Polankhulapo pa mwambowu, bambo Felix Tembo, omwe ndi mkulu woyang'anila ndondomeko zakapelekedwe kangongole ku bungwe la MEDF wati bungweli lidzipeleka powonetsetsa kuti a Malawi akhale odzidalila pa chuma "ife tili okonzeka kupeleka ngongole kwa m’Malawi aliyense potsatila ndondomeko zoyenela”.
Mmawu awo Mfumu yayikulu Khosolo, yalimbikitsa anthu amdera mwawo kuti akatenge ngongole za MEDF kuti akulitse ma business awo ndikusintha miyoyo yawo pa nkhani za chuma, iwo alimbikitsanso anthuwa kuti adzibweza ngongolezi akatenga "ngongole ya MEDF mukuyenera kubweza kuti anzanu enaso apindule nawo."
Bwana nkubwa wa khonsolo ya Mbelwa bambo Emmanuel Bulukutu, anayamikila bungwe la MEDF ponena kuti ngongolezi zithandizila achinyamata komaso amayi pa mabizinezi awo.
Bungweli lati likupelekanso ngongole za Community Development Fund (CDF) zimene ndi za achinyamata komanso azimayi.